Mulungu sanabweretse masoka amene anafuna kubweretsa
ku Nineve chifukwa iwo analapa moona
mtima ngakhale kuti anatsatira milungu ina
ndi kuzunza Aisiraeli.
Pamene wachifwamba wa kumanja ndi mwana
woloŵerera amene anasiya atate wake analapa,
iwo analandira madalitso.
Kupyolera mu zonsezi, Mulungu anasonyeza anthu
kuti angathe kupeŵa masoka ndi kupulumutsidwa
akalapa machimo awo.